Albert Chigoga watsusa mphekesera zoti masapota asankha osewera apamwamba ku Bullets – Zampirampira.com – Football, Netball, Basketball, Hockey,Tennis and sports in Malawi

Albert Chigoga watsusa mphekesera zoti masapota asankha osewera apamwamba ku Bullets

Albert Chigoga watsusa mphekesera zoti masapota asankha osewera apamwamba ku Bullets
Share Button

Mmodzi mwa ma membala akuluakulu a team ya Nyasa Big Bullets a Albert Chigoga watsutsa mphekesera zomwe zikumveka zokuti timuyi ipereka mwayi kwamasapota kuti asankhe osewera omwe achita bwino mu mpikisana wa TNM ligi wa chaka chino.

Mphekeserayi yinamveka kwambiri kucha kwa tsiku lalero, 20 Novembala, 2018, ndipo anthu ayikamba kwambiri mmasamba osiyanasiyana a amchezo, monga Facebook ndi Whatsapp.

Poyankhulana ndi mkuluyu, iye wati ngati kuli kutelo achita kulengeza mwapaderadera kudzera mumsonkhano wa atolankhani.

“Tichita kunena mwatchutchutchu ngati kuli kuchita motelomo. Tiyitanitsa msonkhano wa atolankhani pokhapokha ngati ku likulu kwa timuyi kuli kokonzeka kuchita motero,” a Chigoga anafotokoza motero.

Mumphekeserazi munakambidwa nkhani yoti magulu otsatilawa ndiomwe azakhale ndimwayi opata mphotho pamavoti amasapotawo: mnyamata woyima pagolo opambana, mnyamata otchinjiriza golo mochititsa kaso, mnyamata yemwe wasewera bwino pakati pa timuyi komanso mmodzi mwa wosewera omwetsa zigoli yemwe wasewera bwino.

Panamvekaso zokuti masapota omwe adzathe kuvota ndiomwe analembetsa ngati mamembala a timuyi.

Share Button

newton

A journalist by profession. Did journalism at Malawi Institute of Journalism. Currently working at Malawi Sports as an online sports journalist.