Tsogolo la mphuzitsi wa mkulu wa Be Forward Wanderers ili pa chiopsezo pamene timuyi sikuchita bwino.
Izi zili chonchi kamba kwa kozagwirizana komwe kukumakhala pakati pa mphuzitsi wa timuyi Edding’itoni Ng’onamo ndi omuthandizila wake Eliya Kananji posakha woti asewere zomwe zikuthandizila kusachita bwino kwa timuyi.
Timuyi yapeza pointi imodzi pa masewero atatu a mu ligi zomwe zapangitsa akuluakulu a timuyi kufufuza chomwe chasitsa mzaye kuti njomvu ithyoke nyanga.
Zinachitika sabata yapitayi pomwe timuyi imasewera ndi Nyasa Big Bullets pomwe awiriwa anayambitsa matimu osiyana zomwe zinapangitsa akuluakulu a timuyi kulowelerapo pa osewera omwe amayenera kuyamba.
Pakanali pano timuyi ikufuna italemba ntchito mwa awa; Ernest Mtawali , Nsanzurwimo Ramahdan, Yassin Osiman komanso Bob Mpimkanjira kuti akhale mphuzitsi wa mkulu.
Leave a Comment